Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 77:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzapfuulira kwa Mulungu ndi mau anga;Kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzandicherezera khutu.

2. Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye:Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka;Mtima wanga unakanakutonthozedwa.

3. Ndikumbukila Mulungu ndipo ndibvutika;Ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.

4. Mundikhalitsa maso;Ndigwidwa mtima wosanena kanthu.

5. Ndinaganizira masiku akale, zaka zakalekale.

6. Ndikumbukila Nyimbo yanga, usiku;Ndilingalira mumtima mwanga;Mzimu wanga unasanthula.

7. Kodi Mulungu adzataya nthawi yonse?Osabwerezanso kukondwera nafe.

8. Cifundo cace calekeka konse konse kodi?Lonjezano lace lidatha kodi ku mibadwo yonse?

9. Kodi Mulungu waiwala kucita cifundo?Watsekereza kodi nsoni zokoma zace mumkwiyo?

10. Ndipo ndinati, Cindilaka ici;Koma ndikumbukila zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 77