2. Pakuona nyengo yace ndidzaweruza molunjika.
3. Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;Ndinacirika mizati yace.
4. Ndinati kwa odzitamandira, Musamacita zodzitamandira;Ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5. Musamakwezetsa nyanga yanu;Musamalankhula ndi khosi louma.
6. Pakuti kukuzaku sikucokera kum'mawa,Kapena kumadzulo, kapena kucipululu,
7. Pakuti Mulungu ndiye woweruza;Acepsa wina, nakuza wina.
8. Pakuti m'dzanja la Yehova muli cikho;Ndi vinyo wace acita thobvu;Cidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako:Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwaNadzagugudiza nsenga zace.