Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 75:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tikuyamikani Inu, Mulungu; Tiyamika, pakuti dzina lanu liri pafupi;Afotokozera zodabwiza zanu,

2. Pakuona nyengo yace ndidzaweruza molunjika.

3. Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;Ndinacirika mizati yace.

4. Ndinati kwa odzitamandira, Musamacita zodzitamandira;Ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;

5. Musamakwezetsa nyanga yanu;Musamalankhula ndi khosi louma.

6. Pakuti kukuzaku sikucokera kum'mawa,Kapena kumadzulo, kapena kucipululu,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 75