18. Mukumbukile ici, Yehova, mdaniyo anatonza,Ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.
19. Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa cirombo;Musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.
20. Samalirani cipanganoco;Pakuti malo amdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo ciwawa.
21. Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi;Wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu.
22. Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha;Kumbukilani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.
23. Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu;Kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakweca kosaleka.