Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 74:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu?Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?

11. Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu?Muliturutse ku cifuwa canu ndipo muwatheretu.

12. Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale,Wocita zakupulumutsa pakati pa dziko lapansi.

13. Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu;Mudaswa mitu ya zoopsa za m'madzi.

14. Mudaphwanya mitu ya livyatanu;Mudampereka akhale cakudya ca iwo a m'cipululu.

15. Mudagawa kasupe ndi mtsinje;Mudaphwetsa mitsinje yaikuru.

16. Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu:Munakonza kuunika ndi dzuwa.

17. Munaika malekezero onse a dziko lapansi;Munalenga dzinja ndi malimwe.

18. Mukumbukile ici, Yehova, mdaniyo anatonza,Ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

19. Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa cirombo;Musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.

20. Samalirani cipanganoco;Pakuti malo amdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo ciwawa.

21. Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi;Wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 74