1. Mulungu, munatitayiranji citayire?Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?
2. Kumbukilani msonkhano wanu, umene munaugula kale,Umene munauombola ukhale pfuko la colandira canu;Phiri La Ziyoni limene mukhalamo.
3. Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha,Zoipa zonse adazicita mdani m'malo opatulika.
4. Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu;Aika mbendera zao zikhale zizindikilo.
5. Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.
6. Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zace zonseNdi nkhwangwa ndi nyundo,
7. Anatentha malo anu opatulika;Anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.
8. Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi;Anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.