Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 74:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu, munatitayiranji citayire?Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?

2. Kumbukilani msonkhano wanu, umene munaugula kale,Umene munauombola ukhale pfuko la colandira canu;Phiri La Ziyoni limene mukhalamo.

3. Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha,Zoipa zonse adazicita mdani m'malo opatulika.

4. Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu;Aika mbendera zao zikhale zizindikilo.

5. Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.

6. Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zace zonseNdi nkhwangwa ndi nyundo,

7. Anatentha malo anu opatulika;Anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.

8. Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi;Anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.

9. Sitiziona zizindikilo zathu;Palibenso mneneri;Ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.

10. Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu?Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?

11. Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu?Muliturutse ku cifuwa canu ndipo muwatheretu.

12. Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale,Wocita zakupulumutsa pakati pa dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 74