9. Pakamwa pao anena zam'mwamba,Ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi.
10. Cifukwa cace anthu ace amabwera kudza kuno:Ndipo cikho codzala ndi madzi acigugudiza.
11. Namati, Akacidziwa bwanji Mulungu?Kodi Wam'mwambamwamba ali nayonzeru?
12. Tapenyani, oipa ndi awa;Ndipo pokhazikika cikhazikikire aonjezerapo pa cuma cao.
13. Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwacabe,Ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa;
14. Popeza andisautsa tsiku lonse,Nandilanga mamawa monse,
15. Ndikadati, Ndidzafotokozera cotere,Taonani, ndikadacita cosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.
16. Pamene ndinayesa kudziwitsa ici,Ndinabvutika naco;
17. Mpaka ndinalowa m'zoyera za Mulungu,Ndi kulingalira citsiriziro cao.
18. Indedi muwaika poterera:Muwagwetsa kuti muwaononge.