26. Likatha thupi langa ndi mtima wanga:Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi colandira canga cosatha.
27. Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka;Muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.
28. Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu:Ndimuyesa Ambuye Yehova pathawirapo ine,Kuti ndifotokozere nchito zanu zonse,