Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 73:13-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwacabe,Ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa;

14. Popeza andisautsa tsiku lonse,Nandilanga mamawa monse,

15. Ndikadati, Ndidzafotokozera cotere,Taonani, ndikadacita cosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.

16. Pamene ndinayesa kudziwitsa ici,Ndinabvutika naco;

17. Mpaka ndinalowa m'zoyera za Mulungu,Ndi kulingalira citsiriziro cao.

18. Indedi muwaika poterera:Muwagwetsa kuti muwaononge.

19. Ha! m'kamphindi ayesedwa bwinja;Athedwa konse ndi zoopsya.

20. Monga anthu atauka, apepula loto;Momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa cithunzithunzi cao.

21. Pakuti mtima wanga udawawa,Ndipo ndinalaswa m'imso zanga;

22. Ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu;Ndinali ngati nyama pamaso panu.

23. Koma ndikhala ndi Inu cikhalire:Mwandigwira dzanja langa la manja.

24. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu,Ndipo mutatero, mudzandilandira m'ulemerero,

25. Ndiri ndi yani Kumwamba, koma Inu?Ndipo Pa dziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.

26. Likatha thupi langa ndi mtima wanga:Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi colandira canga cosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 73