Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 73:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cifukwa cace anthu ace amabwera kudza kuno:Ndipo cikho codzala ndi madzi acigugudiza.

11. Namati, Akacidziwa bwanji Mulungu?Kodi Wam'mwambamwamba ali nayonzeru?

12. Tapenyani, oipa ndi awa;Ndipo pokhazikika cikhazikikire aonjezerapo pa cuma cao.

13. Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwacabe,Ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa;

14. Popeza andisautsa tsiku lonse,Nandilanga mamawa monse,

15. Ndikadati, Ndidzafotokozera cotere,Taonani, ndikadacita cosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.

16. Pamene ndinayesa kudziwitsa ici,Ndinabvutika naco;

17. Mpaka ndinalowa m'zoyera za Mulungu,Ndi kulingalira citsiriziro cao.

18. Indedi muwaika poterera:Muwagwetsa kuti muwaononge.

19. Ha! m'kamphindi ayesedwa bwinja;Athedwa konse ndi zoopsya.

20. Monga anthu atauka, apepula loto;Momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa cithunzithunzi cao.

21. Pakuti mtima wanga udawawa,Ndipo ndinalaswa m'imso zanga;

22. Ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu;Ndinali ngati nyama pamaso panu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 73