Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 73:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Indedi Mulungu acitira Israyeli zabwino,Iwo a mtima wa mbe.

2. Koma ine, ndikadagwa; Mapazi anga akadaterereka,

3. Pakuti ndinacitira nsanje odzitamandira,Pakuona mtendere wa oipa,

4. Pakuti palibe zomangira pakufa iwo:Ndi mphamvu yao niolimba,

5. Sabvutika monga anthu ena;Sasautsika monga anthu ena.

6. Cifukwa cace kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao;Acibvala ciwawa ngati malaya.

7. Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao:Malingaliro a mitima yao asefukira.

8. Acita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa:Alankhula modzitama.

9. Pakamwa pao anena zam'mwamba,Ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 73