1. Indedi Mulungu acitira Israyeli zabwino,Iwo a mtima wa mbe.
2. Koma ine, ndikadagwa; Mapazi anga akadaterereka,
3. Pakuti ndinacitira nsanje odzitamandira,Pakuona mtendere wa oipa,
4. Pakuti palibe zomangira pakufa iwo:Ndi mphamvu yao niolimba,
5. Sabvutika monga anthu ena;Sasautsika monga anthu ena.
6. Cifukwa cace kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao;Acibvala ciwawa ngati malaya.
7. Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao:Malingaliro a mitima yao asefukira.
8. Acita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa:Alankhula modzitama.