Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 71:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndikhulupirira Inu, Yehova:Ndisacite manyazi nthawi zonse.

2. Ndikwatuleni m'cilungamo canu, ndi kundilanditsa:Ndicherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.

3. Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;Mwalamulira kundipulumutsa;Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,

4. Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa,M'dzanja la munthu wosalungama ndi waciwawa.

5. Pakuti Inu ndinu ciyembekezo canga, Ambuye Yehova;Mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

6. Inu munandigwirizizakuyambira ndisanabadwe:Kuyambira pa thupi la mai wanga wondicitira zokoma ndinu;Ndidzakulemekezani kosalekeza.

7. Ndikhala codabwiza kwa ambiri;Koma Inu ndinu pothawira panga polimba.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 71