1. Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu:Mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;
2. Kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,Ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.
3. Yehova Mulungu wanga, ngati ndacita ici;Ngati m'manja anga muli cosalungama;
4. Ngati ndambwezera coipa iye woyanjana ndine;(Inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda cifukwa);
5. Mdani alondole moyo wanga, naupeze;Naupondereze pansi moyo wanga,Naukhalitse ulemu wanga m'pfumbi.
6. Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,Nyamukani cifukwa ca ukali wa akundisautsa:Ndipo mugalamukire ine; mwalamulira ciweruzo.