Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 7:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu:Mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

2. Kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,Ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.

3. Yehova Mulungu wanga, ngati ndacita ici;Ngati m'manja anga muli cosalungama;

4. Ngati ndambwezera coipa iye woyanjana ndine;(Inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda cifukwa);

5. Mdani alondole moyo wanga, naupeze;Naupondereze pansi moyo wanga,Naukhalitse ulemu wanga m'pfumbi.

6. Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,Nyamukani cifukwa ca ukali wa akundisautsa:Ndipo mugalamukire ine; mwalamulira ciweruzo.

7. Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;Ndipo pamwamba pao mubwerere kumka kumwamba.

8. Yehova aweruza anthu mlandu:Mundiweruze, Yehova, monga mwa cilungamo canga, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.

9. Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse:Pakuti woyesa mitima ndi imso ndiye Mulungu wolungama.

10. Cikopa canga ciri ndi Mulungu, Wopulumutsa oongoka mtima.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 7