Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 69:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;Ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.

6. Iwo akuyembekeza Inu, Ambuve Yehova wa makamu, asacite manyazi cifukwa ca ine:Iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israyeli, asapepulidwe cifukwa ca ine.

7. Pakuti ndalola cotonza cifukwa ca Inu:Cimpepulo cakuta nkhope yanga,

8. Abale anga andiyesa mlendo,Ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.

9. Pakuti cangu ca pa nyumba yanu candidya;Ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.

10. Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.

11. Ndipo cobvala canga ndinayesa ciguduli,Koma amandiphera mwambi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 69