15. Cigumula cisandifotsere,Ndipo cakuya cisandimize;Ndipo asanditsekere pakamwa pace pa dzenje.
16. Mundiyankhe Yehova; pakuti cifundo canu ncokoma;Munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
17. Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;Pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.
18. Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;Ndipulumutseni cifukwa ca adani anga,
19. Mudziwa cotonza canga, ndi manyazi anga, ndi cimpepulo canga:Akundisautsa ali pamaso panu,
20. Cotonza candiswera mtima, ndipo ndidwala ine;Ndipo ndinayembekeza wina wondicitira cifundo, koma palibe;Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
21. Ndipo anandipatsa ndulu ikhale cakudya canga;Nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
22. Gome lao likhale msampha pamaso pao;Pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe.
23. M'maso mwao mude, kuti asapenye;Ndipo munjenjemeretse m'cuuno mwao kosalekeza.
24. Muwatsanulire mkwiyo wanu, Ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.
25. Pokhala pao pakhale bwinja;M'mahema mwao musakhale munthu.
26. Pakuti alondola amene Inu munampanda;Ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.
27. Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao;Ndipo asafikire cilungamo canu.
28. Afafanizidwe m'buku lamoyo,Ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama,