Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 69:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipulumutseni Mulungu;Pakuti madzi afikira moyo wanga.

2. Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo;Ndalowa m'madzi ozama, ndipo cigumula candimiza.

3. Ndalema ndi kupfuula kwanga; kum'mero kwauma gwa:M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

4. Ondida kopanda cifukwa acuruka koposa tsitsi la pamutu panga;Ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu:Pamenepo andibwezetsa cosafunkha ine.

5. Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;Ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.

6. Iwo akuyembekeza Inu, Ambuve Yehova wa makamu, asacite manyazi cifukwa ca ine:Iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israyeli, asapepulidwe cifukwa ca ine.

7. Pakuti ndalola cotonza cifukwa ca Inu:Cimpepulo cakuta nkhope yanga,

8. Abale anga andiyesa mlendo,Ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.

9. Pakuti cangu ca pa nyumba yanu candidya;Ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.

10. Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 69