Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 65:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzacita mantha cifukwa ca zizindikilo zanu; Mukondweretsa apo paturukira dzuwa, ndi apo lilowera.

9. Muceza nalo dziko lapansi, muhthirira,Mulilemeza kwambiri;Mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi:Muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.

10. Mukhutitsa nthaka yace yolima;Mufafaniza nthumbira zace?Muiolowetsa ndi mbvumbi;Mudalitsa mmera wace.

11. Mubveka cakaci ndi ukoma wanu;Ndipo mabande anu akukha zakuca.

12. Akukha pa mabusa a m'cipululu;Ndipo mapiri azingika naco cimwemwe.

13. Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;Ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;Zipfuula mokondwera, inde ziyimbira.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 65