Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 65:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Mphulupulu zinandilaka;Koma mudzafafaniza zolakwa zathu.

4. Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,Akhale m'mabwalo anu:Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu,Za m'malo oyera a Kacisi wanu.

5. Mudzatiyankha nazo zoopsa m'cilungamo,Mulungu wa cipulumutso cathu;Ndinu cikhulupiriko ca malekezero Onse a dziko lapansi,Ndi ca iwo okhala kutali kunyanja:

6. Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;Pozingidwa naco cilimbiko.

7. Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ace,Ndi phokoso la mitundu ya anthu.

8. Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzacita mantha cifukwa ca zizindikilo zanu; Mukondweretsa apo paturukira dzuwa, ndi apo lilowera.

9. Muceza nalo dziko lapansi, muhthirira,Mulilemeza kwambiri;Mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi:Muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.

10. Mukhutitsa nthaka yace yolima;Mufafaniza nthumbira zace?Muiolowetsa ndi mbvumbi;Mudalitsa mmera wace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 65