1. M'Ziyoni akulemekezani Inu mwacete, Mulungu:Adzakucitirani Inu cowindaci.
2. Wakumva pemphero Inu,Zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.
3. Mphulupulu zinandilaka;Koma mudzafafaniza zolakwa zathu.
4. Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,Akhale m'mabwalo anu:Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu,Za m'malo oyera a Kacisi wanu.
5. Mudzatiyankha nazo zoopsa m'cilungamo,Mulungu wa cipulumutso cathu;Ndinu cikhulupiriko ca malekezero Onse a dziko lapansi,Ndi ca iwo okhala kutali kunyanja: