6. Pokumbukira Inu pa kama wanga,Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.
7. Pakuti munakhala mthandizi wanga;Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.
8. Moyo wanga uumirira Inu:Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.
9. Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,Adzalowa m'munsi mwace mwa dziko.
10. Adzawapereka ku mphamvu ya lupanga;Iwo adzakhala gawo la ankhandwe.
11. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;Yense wakulumbirira iye adzatamandira;Pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.