Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 63:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kuca:Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu,M'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

2. Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,Monga ndinakuonani m'malo oyera.

3. Pakuti cifundo canu ciposa moyo makomedwe ace;Milomo yanga idzakulemekezani.

4. Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;Ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

5. Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;Ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakupfuula mokondwera;

6. Pokumbukira Inu pa kama wanga,Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7. Pakuti munakhala mthandizi wanga;Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8. Moyo wanga uumirira Inu:Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9. Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,Adzalowa m'munsi mwace mwa dziko.

10. Adzawapereka ku mphamvu ya lupanga;Iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 63