Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 60:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;Mwakwiya; tibwezereni.

2. Mwagwedeza dziko, mwaling'amba:Konzani ming'alu yace; pakuti ligwedezeka.

3. Mwaonetsa anthu anu zowawa:Mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.

4. Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,Aikweze cifukwa ca coonadi.

5. Kuti okondedwa anu alanditsidwe,Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutibvomereze.

6. Mulungu walankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera:Ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.

7. Gileadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;Ndipo Efraimu ndi mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga,

8. Moabu ndiye mkhate wanga;Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga:Filistiya, pfuulatu cifukwa ca ine.

9. Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?

10. Si ndinu, Mulungu, amene mwantaya?Osaturuka nao makamu athu, Mulungu.

11. Tithandizeni kunsautso;Kuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.

12. Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima,Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 60