Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 59:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;Mudzalalatira amitundu onse.

9. Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani;Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.

10. Mulungu wa cifundo canga adzandikumika:Adzandionetsa tsoka la adani anga.

11. Musawapheretu, angaiwale anthu anga:Muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,Ambuye, ndinu cikopa cathu.

12. Pakamwa pao acimwa ndi mau onse a pa milomo yao,Potero akodwe m'kudzitamandira kwao,Ndiponso cifukwa ca kutemberera ndi bodza azilankhula.

13. Muwathe mumkwiyo, muwagurule psiti:Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo,Kufikira malekezero a dziko la pansi.

14. Ndipo abwere madzulo, auwe ngati garu,Nazungulire mudzi.

15. Ayendeyende ndi kufuna cakudya,Nacezere osakhuta.

16. Koma ine, ndidzayimbira mphamvu yanu;Inde ndidzayimbitsa cifundo canu mamawa:Pakuti Inu mwakhala msanje wanga,Ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.

17. Ndidzayimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga:Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa cifundo canga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 59