Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 59:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga:Ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.

2. Mundilanditse kwa ocita zopanda pace,Ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.

3. Pakuti onani, alalira moyo wanga;Amphamvu andipangira ciwembu:Osacimwa, osalakwa ine, Yehova,

4. Osawapatsa cifukwa ine, athamanga nadzikonza;Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.

5. Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli,Ukani kukazonda amitundu onse:Musacitire cifundo mmodzi yense wakucita zopanda pace monyenga.

6. Abwera madzulo, auwa ngati garu,Nazungulira mudzi.

7. Onani abwetuka pakamwa pao;M'milomo mwao muli lupanga,Pakuti amati, Amva ndani?

8. Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;Mudzalalatira amitundu onse.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 59