Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 57:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mundicitire cifundo, Mulungu, mundicitire cifundo;Pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu:Ndipo ndithawira ku mthunzi wa mapiko anu,Kufikira zosakazazo zidzapita.

2. Ndidzapfuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba;Ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.

3. Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsaPonditonza wofuna kundimeza;Mulungu adzatumiza cifundo cace ndi coonadi cace.

4. Moyo wanga uli pakati pa mikango;Ndigona pakati pa oyaka moto,Ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mibvi,Ndipo lilime lao ndilio lupanga lakuthwa.

5. Mukwezeke m'mwambamwa mba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.

6. Anandichera ukonde apo ndiyenda;Moyo wanga wawerama:Anandikumbira mbuna patsogolo panga;Anagwa m'kati mwace iwo okha.

7. Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;Ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.

8. Galamuka, ulemu wanga; galamukani cisakasa ndi zeze:Ndidzauka ndekha mamawa.

9. Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye:Ndidzakuyimbirani mwa mitundu.

10. Pakuti cifundo canu ncacikuru kufikira m'mwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 57