Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 56:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mundicitire cifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza:Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.

2. Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse:Pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.

3. Tsiku lakuopa ine,Ndidzakhulupirira Inu.

4. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;Anthu adzandicitanji?

5. Tsiku lonse atenderuza mau anga:Zolingirira zao zonse ziri pa ine kundicitira coipa.

6. Amemezana, alalira,Achereza mapazi anga,Popeza alindira moyo wanga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 56