Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 55:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,Tsamwali wanga, wodziwana nane.

14. Tinapangirana upo wokoma,Tinaperekeza khamu la anthu popita ku nyumba ya Mulungu.

15. Imfa iwagwere modzidzimutsa,Atsikire kumanda ali amoyo:Pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao,

16. Koma ine ndidzapfuulira kwa Mulungu;Ndipo Yehova atizandipulumutsa.

17. Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,Ndipo adzamva mau anga.

18. Anaombola moyo wanga ku nkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere:Pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

19. Mulungu adzamva, nadzawasautsa,Ndiye wokhalabe ciyambire kale lomwe.Popeza iwowa sasinthika konse,Ndipo saopa Mulungu.

20. Anaturutsa manja ace awagwire iwo akuyanjana naye:Anaipsa pangano lace.

21. Pakamwa pace mposalala ngati mafuta amkaka,Koma mumtima mwace munali nkhondo:Mau ace ngofewa ngati mafuta oyenga,Koma anali malupanga osololasolola.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 55