Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 52:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Udzitamandiranji ndi coipa, ciphonaiwe?Cifundo ca Mulungu cikhala tsiku lonse.

2. Lilime lako likupanga zoipa;Likunga lumo lakuthwa, lakucita monyenga.

3. Ukonda coipa koposa cokoma;Ndi bodza koposa kunena cilungamo.

4. Ukonda mau onse akuononga, Lilime lacinyengo, iwe.

5. Potero Mulungu adzakupasula ku nthawi zonse,Adzakucotsa nadzakukwatula m'hema mwako,Nadzakuzula, kukucotsa m'dziko la amoyo.

6. Ndipo olungama adzaciona, nadzaopa,Nadzamseka, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 52