1. Udzitamandiranji ndi coipa, ciphonaiwe?Cifundo ca Mulungu cikhala tsiku lonse.
2. Lilime lako likupanga zoipa;Likunga lumo lakuthwa, lakucita monyenga.
3. Ukonda coipa koposa cokoma;Ndi bodza koposa kunena cilungamo.
4. Ukonda mau onse akuononga, Lilime lacinyengo, iwe.
5. Potero Mulungu adzakupasula ku nthawi zonse,Adzakucotsa nadzakukwatula m'hema mwako,Nadzakuzula, kukucotsa m'dziko la amoyo.