Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 5:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mverani mau anga, Yehova,Zindikirani kulingirira kwanga.

2. Tamvetsani mau a kupfuula kwanga,Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga:Pakuti kwa Inu ndimapemphera,

3. M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga;M'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.

4. Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera naco coipaMphulupulu siikhala ndi Inu.

5. Opusa sadzakhazikika pamaso panu:Mudana nao onse akucita zopanda pace.

6. Mudzaononga iwo akunena bodza:Munthu wokhetsa mwazi ndi wacinyengo, Yehova anyansidwa naye.

7. Koma ine, mwa kucuruka kwa cifundo canu ndidzalowa m'nyumba yanu:Ndidzagwada kuyang'ana Kacisi wanu woyera ndi kuopa Inu.

8. Yehova, munditsogolere m'cilungamo canu, cifukwa ca akundizondawo;Mulungamitse njira yanu pamaso panga.

9. Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika;M'kati mwao m'mosakaza;M'mero mwao ndi manda apululu:Lilime lao asyasyalika nalo.

10. Muwayese otsutsika Mulungu;Agwe nao uphungu wao:M'kucuruka kwa zolakwa zao muwapitikitse;Pakuti anapikisana ndi Inu.

11. Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,Apfuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;Nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.

12. Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;Mudzamcinjiriza naco cibvomerezo ngati cikopa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 5