Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 48:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Phiri la Ziyoni, cikhalidwe cace ncokomaKu mbali zace za kumpoto,Ndilo cimwemwe ca dziko lonse lapansi,Mudzi wa mfumu yaikuru.

3. Mulungu adziwika m'zinyumba zace ngati msanje.

4. Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,Anapitira pamodzi.

5. Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;Anaopsedwa, nathawako.

6. Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;Anamva cowawa, ngati wam'cikuta.

7. Muswa zombo za ku Tarisi ndi mphepo ya kum'mawa.

8. Monga tidamva, momwemo tidapenyaM'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu:Mulungu adzaukhazikitsa ku nthawi yamuyaya.

9. Tidalingalira za cifundo canu, Mulungu,M'kati mwa Kacisi wanu.

10. Monga dzina lanu, Mulungu,Momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi:M'dzanja lamanja lanu mudzala cilungamo.

11. Likondwere phiri la Ziyoni,Asekere ana akazi a Yuda,Cifukwa ca maweruzo anu.

12. Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge;Werengani nsanja zace.

13. Penyetsetsani malinga ace,Yesetsani zinyumba zace;Kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.

14. Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthawi za nthawi:Adzatitsogolera kufikira imfa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 48