Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 48:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,M'mudzi wa Mulungu wathu, m'phiri lace loyera.

2. Phiri la Ziyoni, cikhalidwe cace ncokomaKu mbali zace za kumpoto,Ndilo cimwemwe ca dziko lonse lapansi,Mudzi wa mfumu yaikuru.

3. Mulungu adziwika m'zinyumba zace ngati msanje.

4. Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,Anapitira pamodzi.

5. Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;Anaopsedwa, nathawako.

6. Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;Anamva cowawa, ngati wam'cikuta.

7. Muswa zombo za ku Tarisi ndi mphepo ya kum'mawa.

8. Monga tidamva, momwemo tidapenyaM'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu:Mulungu adzaukhazikitsa ku nthawi yamuyaya.

9. Tidalingalira za cifundo canu, Mulungu,M'kati mwa Kacisi wanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 48