Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 47:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Mulungu wakwera ndi mpfuu,Yehova ndi liu la lipenga.

6. Yimbirani Mulungu, yimbirani;Yimbirani Mfumu yathu, yimbirani.

7. Pakuti Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi;Yimbirani ndi cilangizo.

8. Mulungu ndiye Mfumu ya amitundu:Mulungu akhala pa mpando wacifumu wace woyera.

9. Akulu a anthu asonkhanaAkhale anthu a Mulungu wa Abrahamu:Pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;Akwezeka kwakukuru Iyeyo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 47