3. Atigonjetsera anthu,Naika amitundu pansi pa mapazi athu.
4. Atisankhira colowa cathu,Cokometsetsa ca Yakobo amene anamkonda.
5. Mulungu wakwera ndi mpfuu,Yehova ndi liu la lipenga.
6. Yimbirani Mulungu, yimbirani;Yimbirani Mfumu yathu, yimbirani.
7. Pakuti Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi;Yimbirani ndi cilangizo.
8. Mulungu ndiye Mfumu ya amitundu:Mulungu akhala pa mpando wacifumu wace woyera.
9. Akulu a anthu asonkhanaAkhale anthu a Mulungu wa Abrahamu:Pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;Akwezeka kwakukuru Iyeyo.