Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 47:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu;Pfuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuyimbitsa.

2. Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa;Ndiye mfumu yaikuru pa dziko lonse lapansi.

3. Atigonjetsera anthu,Naika amitundu pansi pa mapazi athu.

4. Atisankhira colowa cathu,Cokometsetsa ca Yakobo amene anamkonda.

5. Mulungu wakwera ndi mpfuu,Yehova ndi liu la lipenga.

6. Yimbirani Mulungu, yimbirani;Yimbirani Mfumu yathu, yimbirani.

7. Pakuti Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi;Yimbirani ndi cilangizo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 47