14. Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,Ndi kuti anthu atipukusire mitu.
15. Tsiku lonse cimpepulo canga cikhala pamaso panga,Ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.
16. Cifukwa ca mau a wotonza wocitira mwano;Cifukwa ca mdani ndi wobwezera cilango,
17. Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,Ndipo sitinacita monyenga m'pangano lanu.
18. Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo,Ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu;
19. Mungakhale munatityola mokhala zirombo,Ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.
20. Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,Ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wacilendo;
21. Mulungu sakadasanthula ici kodi?Pakuti adziwa zinsinsi za mtima.