Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 44:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mutibwereretsa kuthawa otisautsa:Ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.

11. Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya;Ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.

12. Mugulitsa anthu anu kwacabe,Ndipo mtengo wace simupindula nao.

13. Mutisandutsa cotonza kwa anzathu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga.

14. Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,Ndi kuti anthu atipukusire mitu.

15. Tsiku lonse cimpepulo canga cikhala pamaso panga,Ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.

16. Cifukwa ca mau a wotonza wocitira mwano;Cifukwa ca mdani ndi wobwezera cilango,

17. Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,Ndipo sitinacita monyenga m'pangano lanu.

18. Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo,Ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu;

19. Mungakhale munatityola mokhala zirombo,Ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 44