Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 4:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakupfuula ine mundiyankhe, Mulungu wa cilungamo canga;Pondicepera mwandikulitsira malo:Ndicitireni cifundo, imvani pemphero langa.

2. Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?Mudzakonda zacabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?

3. Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayoAdzamva Yehova m'mene ndimpfuulira Iye,

4. Citani cinthenthe, ndipo musacimwe:Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale cete.

5. Iphani nsembe za cilungamo,Ndipo mumkhulupirire Yehova.

6. Ambiri amati, Adzationetsa cabwino ndani?Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

7. Mwapatsa cimwemwe mumtima mwanga,Cakuposa cao m'nyengo yakucuruka dzinthu zao ndi vinyo wao.

8. Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;Cifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 4