5. Yehova, m'mwambamuli cifundo canu;Coonadi canu cifikira kuthambo.
6. Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu;Maweruzo anu akunga cozama cacikuru:Yehova, musunga munthu ndi nyama.
7. Ha! cifundo canu, Mulungu, ncokondedwadi!Ndipo ana a anthu athawira ku mthunzi wa mapiko anu.
8. Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu:Ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.
9. Pakuti citsime ca moyo ciri ndi Inu:M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.
10. Tanimphitsani cifundo canu pa iwo akudziwa Inu;Ndi cilungamo canu pa oongoka mtima.