Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 36:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakud adzidyoletsa yekha m'kuona kwace,Kuti anthu sadzacipeza coipa cace ndi kukwiya naco.

3. Mau a pakamwa pace ndiwo opanda pace ndi onyenga:Waleka kuzindikira ndi kucita bwino.

4. Alingirira zopanda pace pakama pace;Adziika panjira posad pabwino;Coipa saipidwa naco.

5. Yehova, m'mwambamuli cifundo canu;Coonadi canu cifikira kuthambo.

6. Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu;Maweruzo anu akunga cozama cacikuru:Yehova, musunga munthu ndi nyama.

7. Ha! cifundo canu, Mulungu, ncokondedwadi!Ndipo ana a anthu athawira ku mthunzi wa mapiko anu.

8. Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu:Ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

9. Pakuti citsime ca moyo ciri ndi Inu:M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.

10. Tanimphitsani cifundo canu pa iwo akudziwa Inu;Ndi cilungamo canu pa oongoka mtima.

11. Phazi la akudzikuza lisandifikire ine,Ndi dzanja la oipa lisandicotse.

12. Pomwepo padagwera ocita zopanda pace:Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 36