14. Ndakhala ine monga ngad iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga:Polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wace.
15. Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi:Akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinacidziwa:Ananding'amba osaleka:
16. Pakati pa onyodola pamadyerero,Anandikukutira mano.
17. Ambuye, mudzapenyerabe nthawi yanji?Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao,Wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
18. Ndidzakuyamikanimumsonkhano waukuru:M'cikhamu ca anthu ndidzakulemekezani.
19. Adani anga asandikondwerere ine monyenga;Okwiya nane kopanda cifukwa asanditsinzinire.
20. Pakuti salankhula zamtendere:Koma apangira ciwembu odekha m'dziko.
21. Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao;Nati, Hede, Hede, diso lathu lidacipenya.
22. Yehova, mudacipenya; musakhale cete:Ambuye, musakhale kutali ndi ine.
23. Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga,Mulungu wanga ndi Ambuye wanga,
24. Mundiweruze monga mwa cilungamo canu, Yehova Mulungu wanga;Ndipo asandisekerere ine.
25. Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo!Asanene, Tammeza iye.
26. Acite manyazi, nadodome iwo akukondwera cifukwa ca coipa cidandigwera:Abvekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
27. Apfuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera naco cilungamo canga:Ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova,Amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wace.
28. Ndipo lilime langa lilalikire cilungamo canu,Ndi lemekezo lanu tsiku lonse.