Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 33:7-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu:Amakundika zakudya mosungiramo.

8. Dziko lonse lapansi liope Yehova:Ponse pali anthu acite mantha cifukwa ca Iye,

9. Pakuti ananena, ndipo cinacitidwa;Analamulira, ndipo cinakhazikika.

10. Yehova aphwanya upo wa amitundu:Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11. Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.

12. Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao;Mtundu womwe anausankha ukhale colandira ca iye yekha.

13. Yehova apenyerera m'mwamba; Aona ana onse a anthu.

14. M'malo akhalamo Iye, amapenya pansiPa onse akukhala m'dziko lapansi;

15. Iye amene akonza mitima ya iwo onse,Amene azindikira zocita zao zonse.

16. Palibe mfumu yoti gulu lalikuru limpulumutsa:Mphamvu yaikuru siicilanditsa ciphona,

17. Kavalo safikana kupulumuka naye:Cinkana mphamvu yace njaikuru sapulumutsa.

18. Taonani, diso la Yehova liri pa iwo akumuopa Iye,Pa iwo akuyembekeza cifundo cace;

19. Kupulumutsa moyo wao kwa imfa,Ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.

20. Moyo wathu walindira Yehova:Iye ndiye thandizo lathu ndi cikopa cathu.

21. Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye,Cifukwa takhulupirira dzina lace loyera.

22. Yehova, cifundo canu cikhale pa ife,Monga takuyembekezani Inu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 33