Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 33:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pfuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima:Oongoka mtima ayenera kulemekeza.

2. Yamikani Yehova ndi zeze:Myimbireni ndi cisakasa ca zingwe khumi.

3. Mumyimbire Iye Nyimbo yatsopano;Muyimbe mwaluso kumveketsa mau.

4. Pakuti mau a Yehova ali olunjika;Ndi nchito zace zonse zikhulupirika.

5. Iye ndiye wakukonda cilungamo ndi ciweruzo:Dziko lapansi ladzala ndi cifundo ca Yehova.

6. Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova;Ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwace khamu lao lonse.

7. Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu:Amakundika zakudya mosungiramo.

8. Dziko lonse lapansi liope Yehova:Ponse pali anthu acite mantha cifukwa ca Iye,

9. Pakuti ananena, ndipo cinacitidwa;Analamulira, ndipo cinakhazikika.

10. Yehova aphwanya upo wa amitundu:Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11. Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.

12. Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao;Mtundu womwe anausankha ukhale colandira ca iye yekha.

13. Yehova apenyerera m'mwamba; Aona ana onse a anthu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 33