1. Pfuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima:Oongoka mtima ayenera kulemekeza.
2. Yamikani Yehova ndi zeze:Myimbireni ndi cisakasa ca zingwe khumi.
3. Mumyimbire Iye Nyimbo yatsopano;Muyimbe mwaluso kumveketsa mau.
4. Pakuti mau a Yehova ali olunjika;Ndi nchito zace zonse zikhulupirika.
5. Iye ndiye wakukonda cilungamo ndi ciweruzo:Dziko lapansi ladzala ndi cifundo ca Yehova.
6. Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova;Ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwace khamu lao lonse.
7. Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu:Amakundika zakudya mosungiramo.
8. Dziko lonse lapansi liope Yehova:Ponse pali anthu acite mantha cifukwa ca Iye,
9. Pakuti ananena, ndipo cinacitidwa;Analamulira, ndipo cinakhazikika.
10. Yehova aphwanya upo wa amitundu:Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.
11. Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.