Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 31:9-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mundicitire cifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine:Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mabvuto,

10. Pakuti moyo wanga watha ndi cisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo:Mphamvu yanga yafoka cifukwa ca kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.

11. Ndakhala cotonza cifukwa ca akundisautsa onse,Inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa coopsa:Iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

12. Ndaiwalika m'mtima monga wakufa:Ndikhala monga cotengera cosweka.

13. Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri,Mantha andizinga:Pondipangira ciwembu,Anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

14. Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova:Ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga,

15. Nyengo zanga ziri m'manja mwanu:Mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

16. Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu:Mundipulumutse ndi cifundo canu.

17. Yehova, musandicititse manyazi; pakuti ndapfuulira kwa Inu:Oipa acite manyazi, atonthole m'manda.

18. Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza,Imene imalankhula mwacipongwe pa olungama mtima,Ndi kudzikuza ndi kunyoza.

19. Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukuru nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu,Kumene munacitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!

20. Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa ciwembu ca munthu:Mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.

21. Wolemekezeka Yehova:Pakuti anandicitira cifundo cace codabwiza m'mudzi walinga.

22. Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundicotsa pamaso panu:Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinapfuulira kwa Inu.

23. Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ace:Yehova asunga okhulupirika,Ndipo abwezera zocuruka iye wakucita zodzitama.

24. Limbikani, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu,Inu nonse akuyembekeza Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 31