Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 31:2-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mundicherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga:Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.

3. Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa;Ndipo cifukwa ca dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.

4. Mundionjole m'ukonde umene anandichera mobisika.Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.

5. Ndipereka mzimu wanga m'dzanja lanu:Mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa coonadi.

6. Ndikwiya nao iwo akusamala zacabe zonama:Koma ndikhulupirira Yehova.

7. Ndidzakondwera ndi kusangalala m'cifundo canu:Pakuti mudapenya zunzo langa;Ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga:

8. Ndipo simunandipereka m'dzanja la mdani;Munapondetsa mapazi anga pali malo.

9. Mundicitire cifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine:Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mabvuto,

10. Pakuti moyo wanga watha ndi cisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo:Mphamvu yanga yafoka cifukwa ca kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.

11. Ndakhala cotonza cifukwa ca akundisautsa onse,Inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa coopsa:Iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

12. Ndaiwalika m'mtima monga wakufa:Ndikhala monga cotengera cosweka.

13. Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri,Mantha andizinga:Pondipangira ciwembu,Anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

14. Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova:Ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga,

15. Nyengo zanga ziri m'manja mwanu:Mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

16. Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu:Mundipulumutse ndi cifundo canu.

17. Yehova, musandicititse manyazi; pakuti ndapfuulira kwa Inu:Oipa acite manyazi, atonthole m'manda.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 31