Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 30:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa,Ndipo simunandikondwetsera adani anga,

2. Yehova, Mulungu wanga,Ndinapfuulira kwa Inu, ndipo munandiciritsa.

3. Yehova munabweza moyo wanga kumanda:Munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.

4. Yimbirani Yehova, inu okondedwa ace,Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.

5. Pakuti mkwiyo wace ukhala kanthawi kokha;Koma kuyanja kwace moyo wonse:Kulira kucezera,Koma mamawa kuli kupfuula kukondwera.

6. Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa,Sindidzagwedezeka nthawi zonse.

7. Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu:Munabisa nkhope yanu; ndinaopa.

8. Ndinapfuulira kwa Inu, Yehova;Kwa Yehova ndinapemba:

9. M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje?Ngati pfumbi lidzayamika Inu? ngati lidzalalikira coonadi canu?

Werengani mutu wathunthu Masalmo 30